corona

Zokhudza COVID-19

Kodi COVID-19 ndi chani?

Matenda a Coronavirus 2019 (CODID-19) - 'CO' amayimira 'Corona', 'VI' amayimira 'Virus', ndipo 'D' amayimira 'Disease' - ndi mtundu wamatenda womwe amayambitsidwa ndi mtundu wa ma vayilasi otchedwa coronavirus.

Kodi zizindikiro za COVID-19 ndi chani?

Zizindikirozi ndi monga:

  • kutentha thupi
  • kukhosomola kukhosi kuli kouma
  • kubanika
  • kumva kutopa

Ngati munthu wadwalika kwambiri, akhoza kumva chibayo komanso kupuma movutikira. Nthawi zina, matendawa akhoza kudzetsa imfa.

Zizindikiro izi sizimasiyana kwenikweni ndi zizindikiro zomwe munthu amakhala nazo akakhala ndi chimfine, chomwe ndichodziwika bwino kuposa COVID-19. N'chifukwa chake munthu ayenera kuyezetsa kuti atsimikize ngati ali ndi COVID-19 kapena ayi. Dziwani kuti njira zopewera COVID-19 ndi zomwe zija - kusamba m'manja kawirikawiri komanso kutsokomolera mkati mwa chigongono kapena utadziphimba ndi kansalu kukamwa ndi pamphuno. Ngati watsokomolera kansalu, n'koyenera kutaya ku dzala kapena kukachapa ndi sopo. Katemera wa chimfine aliko, kotero ndikofunika kuti inu ndi mwana wanu mudzionetsetsa kuti mwalandira katemerayu.

Kodi COVID-19 amafala bwanji?

Kavayilasi koyambitsa COVID-19 kamafala kudzera m'malovu kapena timamina ta munthu yemwe ali ndi matendawa (ngati munthuyu akuyetsemula, kutsokomola, kuyimba, kapena kuyankhula) ndipo timalovu ndi timaminato tagwera mudiso, mkamwa kapena m'maso mwa munthu yemwe ali pafupi. Munthu atha kutengaso kachilomboka pogwira kukamwa, m'mphuno kapena m'maso ngati munthuyu anagwira malo pomwe panagwera kavayilasi ka corona. Ka vayilasi ka corona kamatha kukhala moyo kakagwera pachinthu kwa maola kapenanso masiku angapo, koma mutha kupha kachiromboka popukuta zinthu zanu ndi mankhwala kapena sopo.

Dziwani kuti munthu atha kufalitsa kavayilasi ka corona nthawi yomwe asanayambe kuwonetsa zizindikiro komanso akayamba kuwonetsa zizindikiro.

Phunzirani komanso Falitsani Zambiri kwa Ena

Kupita patsogolo