budgeting

Kapangidwe ka Bajeti Yapabanja Panu.

Bajeti ndi chani?

Bajeti ndi dongosolo la kagwiritsidwe ntchito ka ndalama lomwe timakonza, ngakhale panthawi yamavuto osiyanasiyana.

Mungapange bwanji bajeti ya banja lanu?

Budgeting without Pictures

1. Fufuzani ngati mungapeze chithandizo m’dera la kwanu.

  • Boma lanu litha kukhala kuti likupereka ndalama, kapena zakudya ku mabanja munyengo iyi ya mliri wa COVID-19.
  • Funsani ngati pali malo ena ake m’dera lanu komwe akupereka chithandizo.

2. Lembani mndandanda wa ndalama zomwe mumagwiritsa ntchito pakadali pano.

  • Tengani pepala ndi cholembera.
  • Kuchuluka kwa ndalama zomwe banja lanu litha kugwiritsa ntchito pogula chakudya ndi zofunikira zina pa mwezi kutha kusiyana mwezi ndi mwezi. Lembani kuchuuka kwa ndalama zomwe banja lanu litha kugwiritsa ntchito mwezi uno!
  • Jambulani zithunzi za zinthu zonse zomwe banja lanu limagula mwezi uliwonse.
  • Pambali pa chithunzi chilichonse, lembani kuchuluka kwa ndalama zomwe mumagwiritsa ntchito kuti mugule chinthucho,ndipo lembaninso kuti pamwezi mumafuna zinthu zomwe mwajambulazo zingati.

3. Kambiranani za zosowa ndi zofuna zanu.

  • Zosowa za munthu: Ndi zinthu ziti ndi ziti zomwe ndi zofunikira kwambiri kuti anthu pa banjapo akhale ndi moyo? (Zitsanzo: chakudya, sopo osambira m’manja, mankhwala).

4. Lembani bajeti yanu.

  • Pezani thumba lodzadza ndi miyala kapena thumba lomwe muli tizidutswa tambiri. Teyerekeze kuti zimenezi ndiye ndalama zanu zomwe mutagwiritse ntchito mwezi uno.
  • Monga banja, pangani chisankho kuti mugwiritsa ntchito ndalamazi pa zithunzi ziti zomwe mwajambula zija, ndipo ikani miyala ija pa zithunzizo.
  • Ngati mungakwanitse kusungapo ndalama ina kuti mudzagwiritse ntchito mtsogolo kapena pa vuto lokugwa mwadzidzidzi, izo zitha kukhala zosangalatsa!
budgeting

Zikomo powerenga! Tsekulani tsamba la intaneti lomwe laikidwa m’munsimu kuti mupereke maganizo anu pa zomwe mwawerenga zokhudza kulera ana.

Kupita patsogolo