Learning Through Play

Kuphunzira Kudzera M’masewera

Chitani masewera awa limodzi ndi ana anu. Masewerawa alipo amitundu yosiyanasiyana: olimbitsa thupi, kukamba nkhani, ndipo ena ndi zoyankhula za msangulutso chabe. Ambiri mwa masewerawa atha kuseweredwa panja ndipo salira kuti mukhale ndi, kapena mugule zinthu zina ndi zina kuti atheke.

MASEWERA OYENDETSA THUPI

1. Kuvina – Kusiya

Ikani nyimbo pa wailesi kapena m’modzi mwa inu atha kuyimba nyimbo ndipo aliyense ayambe kuvina. Nyimboyo ikangosiya, aliyense apezeke kuti wasiya kuvina nthawi yomweyo ndipo asasunthe. Yemwe apezeke akuvinabe amakhala kuti walephera ndipo ndi amene amatsogolera masewerawa kuvina kukamayambanso.

2. Gule wa Zinyama

Masewerawa sakusiyana kwambiri ndi masewera a Kuvina – Kusiya, koma kuti nyimbo ija ikasiya, aliyense akuyenera kutchula dzina la nyama yomwe angafune ndipo asanduke nyama watchulayo.

3. Galasi

Tsatizirani momwe anzanu akuonekera, akuyendera, kapena akumvekera mawu. Munthu m’modzi akhoza kukhala wotsogolera kenako n’kusinthana mbali ndi mzakeyo. Tayeserani kuchita masewerawa popanda otsogolera!

4. Zip Zap Zop

Ana ayime mozungulira ndipo akuyenera kudumpha ndi kuomba m’manja n’kumatchula mawu oti “ZIP”. Akatero, mwana mmodzi akuyenera kuloza mwana wina pagulupo. Mwana yemwe walozedwayo akuyenera kudumpha, kuomba mmanja, kenako kuloza n’kutchula mawu woti “ZAP”. Mwana wolozedwayonso achite chimodzimodzi koma iye atchula mawu oti “ZOP”. Izi zipitirire mpaka mmodzi mwa anawo atatchula mawu olakwika, kapena kusokoneza kadumphidwe ndi kaombedwe ka mmanja (polephera kudumpha kapena kudumpha mochedwa).

5. Mtsogoleri ndi ndani?

Gwedezani thupi lanu kangapo motsogozana. Gwedezani pang’onopang’ono kuti ana/achinyamatawo akhale ndi mwayi oonerera ndi kutsatira. Ena mwa magwedezedwe amene mungachite ndi awa: kukweza manja ndikumakupiza, kenako n’kuwerama uku mukugwira zala zanu zakuphazi, n’kuimirira ndi mwendo umodzi omwe zala zake zaloza mkati mwa bwalo lomwe mwapanga. Sankhani munthu mmodzi kuti ayambe wachoka pa bwalopo kwa kanthawi kochepa, kapena aphimbe kunkhope kwake ndi china chake. Sankhani mwana kapena wachisodzera wina kuti akhale “mphunzitsi” watsopano. Ana/achisodzerawo ayambe kutsatira zomwe “mphunzitsi” watsopanoyo adzichita. Mmene izi zikuchitika, muuzeni uja anachoka kaye kapena kudziphimba kunkhope uja kuti abwere kapena ayang’ane, ndipo atchule muthu yemwe akutsogolera pa masewerawo. Atha kutchula anthu angapo mpaka atchule mphunzitsi wolondola.

6. Lowezani Kavinidwe kanga!

Mmodzi wa inu ayambe masewerawa posonyeza mtundu wa kavinidwe umene amatha, monga kuponda pansi mwa mdidi, kudumphira m’mwamba, kapena kuvina mozungulira. Woyandikana naye yemwe ali kumanja atsanzire kavinidweko kenako avine mwa mtundu wakewake. Munthu wachitatu amene wayandikira atsatizire kavinidweko ndipo izi zipitirire mpaka aliyense akhale atavinapo. Ana kapena achinyamata achisodzera akuyenera kuyesa kuchita masewerawa mozungulira bwalo lonselo koma pasakhale ophonyetsa. Munthu womaliza ndi amene akuyenera kuloweza kavinidwe ka mitundu yambiri kuposa aliyense.

7. Zifaniziro

Poyambirira penipeni, uzani ana kuti ayendeyende m’chipindamo manja awo akulendewera komanso akupukusa makosi ndi mitu yawo pang’onopang’ono. Pakadutsa masekondi 10 kapena 15, tchulani mawu amodzi. Mukatero, aliyense akuyenera kuyima nthawi yomweyo koma mofanizira tanthauzo la mawu omwe atchulidwawo. Mwachitsanzo, ngati mawu omwe anatchulidwa ndi “kondwera”, aliyense ayime nthawi yomweyo ndikusonyeza momwe munthu “wokondwera” amaonekera. Bwerezani izi kangapo. Ena mwa mawu oonjezera omwe mungatchule ndi monga awa: topa, mantha, sinza, kondwa, ndi ena.

8. Kuvina pa Pepala

Yambani masewerawa pouza anawo kuti akhale awiriawiri. Gulu lililonse la ana awiri liime pa pepala limodzi. Fotokozani kuti ana awiriwo akuyenera kuvina pa pepalalo. Ngati mmodzi mwa awiriwa wagunda pansi povina ndiye kuti awiri onsewo achotsedwa pa masewerawa. Ikani nyimbo pa wayilesi, pa foni kapena kapena muntha kumangoomba m’manja kapena ana onse atha kuimba nyimbo pamodzi. Thimitsani nyimbo ya pa wayilesi ija kapena siyani kuyimba pakadutsa masekondi 30 kapena 40. Uzani anawo kuti apinde pepala amavinirapolo pakati. (Pochita izi, ayambe achoka kaye pa pepalapo). Kenako abwererenso pa pepalapo. Ikaninso nyimbo pa wayilesi ndipo auzeni anawo kuti ayambenso kuvina ali awiriawiri. Pakadutsa pafupifupi masekondi 30, thimitsani wayilesi ija. Kenako, auzeni achinyamatawo kuti apindenso pepala amavinirapo lija pakati ndipo ikaninso nyimbo ija kuti apitirize kuvina.

Learning Through Play

KUKAMBA NKHANI

1. Auzeni ana anuwo nkhani ya ku ubwana wanu

2. Kambani nkhani

Mutha kupeka nkhani yatsopano. Nenani izi: “Tsopano tipeka nkhani, chiganizo chimodzichimodzi. Wina aliyense adzionjezera chiganizo chimodzi ku nkhani imeneyi.” Fotokozani: Pamapeto pa chiganizo chomwe wina aliyense waonjezera, munthuyo adzinena, “MWADZIDZIDZI.” ndipo munthu yemwe wayandikana naye adzipitiriza chiganizocho pamapeto pake n’kunenanso kuti “MWADZIDZIDZI...” Mwachitsanzo, mutha kunena kuti “Ndinanyamuka kuti ndikatenge madzi pomwe MWADZIDZI...” ndipo munthu yemwe ali pafupi amalizitse chiganizocho. Mwachitsazo, pomalizitsa chiganizochi atha kunena kuti “...chinjoka chachikulu chinavumbuluka kuchokera patchire ndipo MWADZIDZIDZI...” Pitirizani mpaka wina aliyense akhale kuti wawonjezera chiganizo chake.

Learning Through Play

MASEWERA OLOTA

1. Zolondola Zitatu ndi Chabodza Chimodzi

Ana amalemba mayina awo komanso zinthu zinayi zokhudza iwo pa pepala lalilkulu. Nenani izi: “pa pepalalo, mukuyenera kulemba zinthu zitatu zomwe zili zoona zokhudza inu komanso chinthu chomodzi chokhudza inu chomwe ndi chabodza. Mwachitsanzo, “Chikondi amakonda kuyimba, kusewera mpira, amatha kuyankhula ziyankhulo khumi ndipo amakonda kuvina.” Ndi chiti mwa zinthu zinayi izi chomwe ndi chabodza? Ana alowe pakati pa bwalo lomwe mwapanga akunyamula mapepala awo aja. Akumane awiriawiri ndikuonetsana zomwe zili pa mapepela awo ndipo aliyense alote chinthu chabodza pa zinthu zinayi zomwe zalembedwa pa pepala la mnzawoyo.

2. Lotani kuti Ndine Ndani

Auzeni anawo kuti akhale modekha pena pake. Aliyense akhale ndi pepala komanso cholembera. Aliyense alembe dzina la munthu wodziwika pa pepalapo. Munene izi: “Lembani dzina la munthu wina wodziwika kwambiri pa zinthu zabwino. Osauza wina aliyense dzina la munthuyo, ndipo mukaona dzina la munthu yemwe mnzanu walemba, musalitchule dzinalo!” Tolelani mapepala onsewo anawo ataima pa mzere. Matani mapepala onse pa msana pa mwana wina aliyense. Onesetsani kuti mwana aliyense asawone dzina lomwe lili pa pepala mwamata pamsana pake. Ntchito ya anawo ndi kulota dzina lomwe lili pa msana pawo. Kuti adziwe kuti dzinalo ndi ndani, akuyenera kuzungulirazungulira n’kumafunsa anzawowo mafunso omwe yankho lake ndi “eya” kapena “ayi” okhudza munthu yemwe walembedwa pa msana pawopo. Ngati akulandira mayankho a “eya”, akhoza kupitiriza kufunsa munthu yemweyo mafunso ena mpakana atayankhidwa kuti “ayi”. Akalandira yankho loti “ayi”, akhoza kukafunsa mafunso munthu wina. Ngati mwana akuwona kuti tsopano atha kudziwa munthu yemwe walembedwa pa pepala lili pamsana pake, achotse pepala lili pa msana ndikumata cha pamtimapa. Kenako, mwanayo alembe dzina lake lenileni pa pepalapo. Mwana ameneyu athandize ana anzake mmene angadziwire dzina lomwe lamatidwa pamsana pawo.

Kubwerera Kupita patsogolo