Nthawi yokumana pamaso mpamaso
Kutsekedwa kwasukulu ndi mwayi wina wopangira ubale wabwino ndi ana athu komanso ana athu achinyamata. Nthawi ya m'modzim'modzi pamaso mpamaso ndi yaulere komanso yosangalatsa. Imapangitsa ana kumva kuti akukondedwa komanso kuti ndiotetezeka, ndikuwawonetsa kuti ndiofunikira.
Patulani nthawi yocheza ndi mwana aliyense
Itha kukhala kwa mphindi 20 zokha, kapena kuposera apo - zili ndi ife. Itha kukhala nthawi yofanana tsiku lililonse kuti ana kapena achinyamata azikhala akuyembekezera mkumanowu.
Funsani mwana wanu zomwe angafune kuchita
Akasankha okha zimapangitsa kuti azidalire pawokha. Ngati akufuna kuchita china chake chomwe sichili CHABWINO kumchitidwe wokhala motalikirana, ndiye kuti uwu ndi mwayi wolankhula nawo za izi.
Ndi khanda lanu komanso mwana wongoyenda kumene
- Tsatirani zomwe akuchita pankhope zawo komanso mawu awo
- Imbani nyimbo, pangani nyimbo ndi miphika ndi masupuni
- Sanjikizani makapu kapena mabuloku
- Fotokozani nkhani, werengani buku, kapena gawani zithunzi
Ndi mwana wanu wachichepere
- Werengani buku kapena onani zithunzi
- Ngati kuli kotetezeka, pitani koyenda panja kapena kuzungulira nyumba yanu
- Vinani nyimbo kapena yimbani nyimbo
- Chitani ntchito limodzi - pangitsani kukonza ndi kuphika kukhala masewera
- Thandizani ntchito ya kusukulu
Ndi mwana wanu wachinyamata
- Lankhulani za zomwe amakonda: masewera, nyimbo, anthu otchuka, abwenzi
- Ngati kuli kotetezeka, pitani koyenda - panja panyumba kapena kuzungulira nyumba yanu
- Chitani masewera olimbitsa thupi limodzi ndi nyimbo zomwe amakonda