Kupanga chizolowezi cha zochita
COVID-19 yachotsa zizolowezi zathu za tsiku ndi tsiku, kunyumba ndi kusukulu.
Izi ndizovuta kwa ana, achinyamata komanso kwa inu. Kupanga zizolowezi zatsopano kungathandize.
Pangani zizolowezi zoti muzichita zatsiku ndi tsiku zosavuta koma zosasintha
- Pangani dongosolo lanu ndi la ana anu lomwe lili ndi nthawi yochitira zinthu zina komanso nthawi yosachita kanthu. Izi zitha kuthandiza ana kumva kukhala otetezeka komanso amakhalidwe abwino.
- Ana kapena achinyamata akhoza kuthandizira kukonza zochita zatsikulo - monga kupanga ndondomeko yazochita za kusukulu. Ana adzazitsatira izi bwino ngati angathandizire kupanga nawo.
- Phatikizani masewera olimbitsa thupi tsiku lililonse - izi zimathandiza kuchotsa nkhawa komanso kuthandiza ana omwe ali ndi mphamvu zambiri kunyumba.
Phunzitsani mwana wanu za kukhala motalikirana motetezeka
- Ngati ndikotetezeka ndikololedwa, pititsani ana panja kuti azikasewera.
- Muthanso kulemba makalata ndi kujambula zithunzi kuti mugawane ndi anthu. Kaikeni kunja kwa nyumba yanu kuti ena awone!
- Mutha kutsimikizira mwana wanu polankhula za momwe mumakhalira otetezeka. Mverani malingaliro awo ndikuwatenga malingaliro mozama.
Pangani kusamba m'manja ndi ukhondo kukhala kosangalatsa
- Pangani nyimbo ya masekondi 20 yosambira m'manja. Onjezani zochita! Apatseni ana malikisi ndi matamando pakusamba m'manja nthawi zonse.
- Pangani masewera kuti muwone ndikangati komwe tingakhudze nkhope zathu ndikupereka mphotho kwa iye amene angakhale ndi nambala yaying'ono yogwirira kumaso (mutha kuwerengerana).
Ndinu chitsanzo kwa khalidwe la mwana wanu
Ngati mumakhala motalikirana ndikudzisamalira nokha, ndikuwonetsa kwa ena chikondi, makamaka kwa iwo amene akudwala kapena osatetezeka - ana anu ndi achinyamata adzaphunzira kuchokera kwa inu.