Kukambirana za COVID-19
Khalani okonzeka kuyankhula. N’kutheka kuti anawo anamvapo kale zina ndi zina. Kukhala chete kapena kusunga zinsinsi sikumateteza ana athu, koma chilungamo ndi kumasukuirana nawo. Ganizirani kuti anawo atha kumvetsetsa zinthu zochuluka motani. Inuyo ndi amene mumawadziwa bwino kwambiri ana anu.
Khalani omasuka ndipo mvetserani Muloleni mwana wanu ayankhule momasuka. Mufunseni mafunso ndipo fufuzani zomwe akudziwa kale.
Khalani achilungamo Yankhani mafunso a ana anu mwachilungamo. Lingalirani kuti mwana wanu ali ndi zaka zingati ndipo ndi zinthu ziti ndi ziti zomwe atha kuzimvetsetsa.
Limbikitsani ana anu Mwana wanu atha kukhala ndi mantha komanso kusokonekera. Apatseni ana anu mwayi wokuuzani momwe akumvera komanso atsimikizireni kuti mutha kuwathandiza pa vuto la mtundu wina uliwonse lomwe anagakhale nalo.
Palibe vuto lina lililonse ngati mulibe mayankho Palibe vuto lina lililonse kunena kuti “ Sitikudziwa, koma tichitapo kanthu; kapena sitikudziwa, ‘koma tikuganiza’. Uwu utha kukhala mwayi wanu woti muphunzire zinthu zatsopano ndi mwana wanu!
Khalani othandiza, osati onyoza ena Fotokozani kuti matenda a COVID-19 samatengera zoti muthu amaoneka bwanji, amachokera kuti, kapena amayankhula chiyankhulo chanji. Muuzeni mwana wanu kuti tikhoza kuwachitira chifundo anthu omwe akudwala matendawa komanso omwe akuwayang’anira.
Pezani nkhani zokhudza anthu omwe akugwira ntchito yothana ndi mliri wa COVID-19 komanso kusamalira anthu odwala.
Malizitsani ndi Zabwino Onani ngati mwana wanu ali bwinobwino. Mutsimikizireni kuti mumamukonda ndipo atha kukambirana nanu nthawi ina iliyonse. Chitani chinthu china chake chosangalatsa limodzi!