Ndingateteze bwanji banja langa ku COVID-19
Zina mwa zomwe inu ndi banja lanu mukuyenera kutsata pofuna kudziteteza ku COVID-19 ndi izi:
- Sambani m'manja pafupipafupi ndi sopo kapena kudzola makhwala ophera majelemusi m'manja.
- Tsekani kukamwa ndi mkati mwa chigongono chanu kapena pogwiritsa ntchito kansalu kapena kapepela potsokomola kapena pomina. Tayani kapepalako mu malo oyenera, kapena chapani ndi sopo ngati kali kansalu.
- Nthawi zonse onsetsetsani kuti mukutalikirana lipande limodzi (mita imodzi) ndi anzanu.
- Pukutani ndi sopo kapena mankhwala zinthu zomwe anthu amakonda kuzigwiragwira monga mafoni, zigwiriro za zitseko, poyatsira magetsi, komanso pamwamba pa matebulo.
- Pezani chithandizo cha kuchipatala ngati inu kapena mwana wanu akumva kutentha thupi, akutsokomola, kapena akubanika popuma komanso kumva zizindikiro zina za COVID-19.
- Pewani kukhala malo achigulu kapena m'zipinda momwe mphepo siikulowa ndikutuluka mokwanira, ndipo mudziyesetsa kukhala motalikirana ndi anthu ena.
- Valani zotchingira pamphuno ndi kukamwa (masiki) nthawi zonse mukatuluka m'nyumba mwanu makamaka ngati mukupita malo omwe ndikovuta kukhala motalikirana ndi anthu ena.
- Onetsetsani kuti zipinda zonse za nyumba kapena ofesi yanu mukulowa ndikutuluka mphweya mokwanira.