Zikhulupiriro
Kavayilasi ka corona katha kufala malo ena aliwonse posatengera kuti ndikozizira kapena ndikotentha. Chachikulu pofuna kupewa kavayilasika ndikusamba m'manja pafupipafupi ndi sopo kapena kudzola mankhwala ophera majeremusi m'manja.
Anthu amene sakusonyeza zizindikiro, kuphatikizapo ana, akhoza kufalitsa kavayilasi ka corona. N'chifukwa chake munthu ukuyenera kuchepetsa zokumanakumana ndi anthu ena komanso kuonetsetsa kuti tikusamba m'manja ndi sopo pafupipafupi.
Pakali pano palibe umboni kapena kafukufuku yemwe akusonyeza kuti udzudzu utha kufalitsa kavayilasi ka corona.
Palibe katemera yemwe atha kuteteza munthu ku kavayilasi ka corona kapena kuchiza munthu ku matenda a COVID-19.
Mankhwala omwe amapha ma jeremusi mthupi (antibiotics) samakwanitsa kupha mavayilasi mthupi koma ma bakiteliya basi. Mankhwala omwe aliko ndiongothandiza pa zizindikiro zomwe munthu akuonetsa.
Aliyense atha kugwidwa ndi matenda a COVID-19, kungoti anthu achikulire komanso omwe ali ndi vuto la matenda ena (monga matenda a shuga, BP, komanso matenda a mtima) amakhala pa chiopsezo chokulirapo chabe.
Ngakhale kuti matenda a COVID-19 anayamba kupezeka mu dziko la China, matendawa samagwira anthu ochokera dziko kapena dera limodzi. Matendawa samaona kuti munthu ukuchokera dziko kapena dera liti, ndiwe wa mtundu wanji, uli ndi zaka zingati, ndiwe wolumala kapena ayi, kapenanso kuti ndiwe mkazi kapena mwamuna.
Kudzithira mankhwala a chlorine kapena mowa sikungaphe kavayilasi ka corona kamenaekalowa kale m'thupi. Kudzithira zinhu zimenezi kutha kubweretsanso mavuto ena pathupi lanu. Gwiritsani ntchito mankwalawa potsuka zinthu zomwe mumazigwiragwira monga momwe mwalangizidwira.
Mutha kuthandiza kuchepetsa kufala kwa kavayilasi ka corona potalikirana ndi anzanu, kusamba m'manja pafupipafupi ndi sopo, kupewa kudzigwira kunkhope, kukhosomolera mkati mwa chigongono, komanso kupewa kuyendayenda.