Malangizo a Kadyedwe Koyenera Munyengo ya COVID-19
Awa ndi ena mwa malangizo omwe mungatsate podyetsa mwana wanu panyengo ino ya COVID-19.
Kodi pali zoyenera kutsata ndikafuna kum'patsa mwana wanga zakudya zina kupatula mkaka wam'mawere munyengo iyi ya COVID-19?
Mkaka wam'mawere ndi umene uli otetezeka kwambiri kwa mwana. Komabe, mikaka ina yoyenera kwa mwana wakhanda, imene imachita kupangidwa, imatha kuperekedwa kwa mwana ngati mayi woyamwitsa wadwala kwambiri ndipo sangathe kuyamwitsa. Mkaka omwe umagulidwa uli osungunula kale udziperekedwa kwa mwana pokhapokha ngati mukudziwa kuti mulibe madzi otetezeka ku majeremusi kapena njira iliyonse yophera majeremusi pa ziwiya zanu. Mutha kumuyambitsa mwana mkaka omwe umakhalitsa usanaonongeke wa UHT akakwanitsa miyezi 6 yakubadwa.
Kodi nditha kumamudyetsa mwana wanga wa miyezi 6 kapena wokulirapo munyengo iyi ya COVID-19?
Inde, mukuyenera kupitiriza kudyetsa mwana wanu zakudya zakasinthasintha pomupatsa zipatso, masamba, mazira, chimanga, nyemba, nsomba ndi nyama tsiku lililonse komanso kumuyamwitsa mpaka atakwanitsa zaka ziwiri. Mudzisamba m'manja pafupipafupi ndipo mudzionetsetsa kuti ana nawonso akusamba m'manja ndi sopo pafupipafupi ndipo adzikhala pakhomo nthawi zonse. Mudzionetsetsanso kuti mukugwiritsa ntchito ziwiya zaukhondo monga mbale, makapu, ndi zina.
Kodi kudya bwino ndikothandiza bwanji mu nyengo iyi ya COVID-19?
Kudya moyenera komanso kuchita masewera olimbitsa thupi ndizothandiza kuti munthu akhale ndi moyo wautali komanso wathanzi.
Kumupatsa mwana mwana mkaka wam'mawere okhaokha kuli ndi phindu lotani?
- Kuyamwitsa kumathandiza ana kuti atetezeke ku matenda ndipo mkaka wa m'mawere ndi chakudya chodalirika chomwe chingathandize ana kuti akule bwino.
- Mkaka wa m'mawere umakhala ndi chkudya komanso madzi omwe amafunikira kwa mwana miyezi 6 yoyambirira.
- Pamiyezi 6 yoyambirira, mwana tisampatse madzi kapena chakudya cha mtundu wina uliwonse.
- Ngakhale nthawi yotentha, mkaka wa m'mawere umapha ludzu la mwana wanu.
- Kumpatsa mwana zakudya kapena zakumwa zina kumachititsa kuti asamayamwe kwambiri, choncho izi zimachepetsa mkaka wam'mawere umene mukutulutsa. Izi zikhotsa kumudwalitsa mwana wanu.
- Mwana titha kum'mwetsa mankhwala ngati azachipatala anena kuti palibe vuto.