parenting with disabilities

Mmene Tingalerere Ana Olumala

Ana onse, kuphatikizapo omwe ndi olumala, amafunikira kuwaonetsera chikondi, ulemu, chisamaliro, komanso kukhala ndi nthawi yokwanira yokhala nawo limodzi.

1. Onetsetsani kuti mwana wanu ndi wotetezedwa

Sungani manambala a foni, omwe mungaimbe patagwa vuto ladzidzidzi pamalo oonekera monga pa fuliji.

2. Perekani chilimbikitso, chikondi, komanso khalani omvetsetsa.

N’kutheka kuti chithandizo chomwe mumapereka kwa mwana wanu sichimakhala chofanana nthawi zonse, ndipo izi zikhoza kuyambitsa mavuto ena oonjezera monga kuchuluka kwa nkhawa komanso kukhumudwa. Mulimbikitseni mwana wanu pomupatsa zinthu zofunikira pamoyo wake komanso kumupatsa mawu achilimbikitso, ndipo mukatere mwanayo adzaona kuti mumamukondadi. Kumuchitira msangala mwana komanso kumuyankhula mopereka chilimbikitso zimathandiza pamoyo wamwanayu!

3. Lumikizanani ndi mwana wanu.

Mukamayankhula ndi mwana wanu, yankhulani naye mogwirizana ndi msinkhu wake. Mukuyenera kuyang’anizana naye maso ndi maso ndipo sonyezani chidwi chofuna kuyankhulana naye. Perekani mpata wokuti mwanayo naye ayankhule zakukhosi kwake. Muonetsetseni, mumvereni, komanso musonyeze kuti mumamumvetsetsa mwana wanu,

4. Limbikitsani khalidwe labwino.

Limbikitsani khalidwe labwino la mwana wanu pomuyamikira pa zinthu zomwe akuchita bwino. Musalimbane kwambiri ndi zinthu zomwe zimamuvuta; yang’anani kuthekera komwe ali nako. Muthandizireni mwana wanu pochita zinthu pokhapokha ngati akusowekeradi chithandizocho. Mukamangokhalira kumuthandiza pa chilichonse adzakula kwambiri ndi moyo wodalira ndipo atha kudzavutika panthawi imene akuyenra kudziimira payekha.

5. Pemphani ena akuthandizireni pamene mungathe kutero

Landiranani udindo olera ana ndi anthu ena akuluakulu m’banja mwanu. Simuli nokha! Lumikizanani ndi anthu omwe akumvetsetsa nyengo zomwe mukudutsamo. Auzeni ena zokhudza zinthu zomwe zikuyenda bwino KOMANSO mavuto omwe mukukumana nawo. Si chinthu chachilendo kukhala ndi nkhawa, mantha, kapenanso wokhumudwa munyengo imeneyi. Dzikondeni nokha ndipo pomani pamene mukuyenera kutero.

6. Konzani dongosolo labwino la zochita atsiku ndi tsiku.

Kukonza dongosolo la zochita za tsiku ndi tsiku kumathandiza mwana wanu kuti adzichita zinthu molimba mtima komanso mopanda nkhawa. Lembani mndandanda wa zinthu zomwe mwana wanu akuyenera kuchita patsiku, ndipo zikhale zinthu zimene akuzidziwa bwino komanso zina zomwe zimamusangalatsa. Muthandizireni mwana wanu kuti adzitha kulumikizana komanso kucheza ndi anzake ndi abale ake kudzera pa foni, kulemba pa makhadi, kapena kujambula zithunzi. Mupatseni mpata mwana wanu kuti asankhe yekha njira yomwe akufuna, ndi cholinga choti asaone kuti mukuchita mukupangira zochita. Izi zimathandizanso kuti asamadzikaikire. Gwiritsani ntchito chiyankhulo chomveka bwino ndipo mupereke malangizo osavuta kumvetsa. Ngati mukugwiritsa chiyankhulo chogwiritsa ntchito zizindikiro (monga masayini ndi zithunzi), onetsetsani kuti zikhalenso zomveka bwino.

Kubwerera Kupita patsogolo