Momwe Tingalerere Ana M’nyumba ndi M’madera momwe Anthu ali Ochulukana
Kuonetsetsa kuti banja lanu ndi lotetezeka komanso lathanzi kutha kukhala kovutirapo ngati mukukhala pamalo omwe pakukhala anthu ambiri. Izi ndi zina mwa zomwe mungachite:
1. Khalani komwe muli - musayendeyende.
- Chepetsani kulowa ndi kutuluka m’nyumba pakhomo panupo
- Tulukani m’nyumba pokhapokha ngati pali zifukwa zokwanira, monga kukagula zakudya kapena kukapeza chithandizo cha mankhwala.
*2. Chitani zolimbitsa thupi tsiku lililonse.
- Limbikitsani ana anu kuti adzichita zolimbitsa thupi zomwe zingatheke kuchita popanda kukumana ndi anthu ena omwe samakhala m’nyumba mwanu.
- Masewera omadumpha, kuvina kapena kuthamanga anthu angapo mozungulira amasangalatsa!
3. Thandizanani kugwira nchito
- Ntchito zapakhomo, yosamalira ana, ndi zina zigawidwe mofanana kwa anthu am’banjamo.
- Konzani dongosolo la magwiridwe antchito la inu ndi anthu ena akuluakulu pakhomopo losonyeza “nthawi yogwira ntchito” ndi “nthawi yopuma.”
- Sizolakwika kupempha ena kuti akuthandizeni ngati mwatopa ndipo mukufuna kupuma!
4. Chitani zotheka kuti kusamba m’manja komanso ukhondo zikhale zosangalatsa kuchita!
- Zitha kukhala zovutirpo kuti mupeze madzi ndi sopo nthawi zina, koma n’zofunika kwambiri kuti mukhale aukhondo, makamaka m’nyumba zomwe mumakhala anthu ochulukirapo, momwe tizilombo toyambitsa matenda monga bakiteliya timafalikira mosavuta.
- Onetsetsani kuti anthu onse m’banja mwanu akusamba m’manja pafupipafupi.
- Alekeni ana kuti adziphunzitsana okhaokha kasambidwe ka m’manja.
- Limbikitsani ana kuti adzipewa kugwira kunkhope.
5. Thandizani ana anu kuti adzikhala motalikirana.
- Afotokozereni ana anu kuti ali ndi udindo oonetsetsa kuti iwo komanso anthu am’dera mwawo ndiotetezeka popewa kuyandikirana ndi anthu ena panyengo imeneyi.
- Onetsetsani kuti mukupereka chidwi chambiri kwa ana anu pamene akuyesetsa kutalikirana ndi anthu ena.
6. Khalani ndi nthawi yopuma.
*Pamene mukumva kutopa kapena kukhumudwa, pumani! Ngakhale kupumira m’mwamba katatu kukhoza kukhala kothandiza kwambiri.
Zikomo kwambiri powerenga zonsezi! Tsekulani tsamba lomwe laikidwa m’munsimu kuti mutiuze maganizo anu pa zomwe mwawernga zokhudza kulera ana.