Kulera Kwabwino
Ana onse amachita zolakwika. Sizachilendo ngati ana atopa, ali ndi njala, akuopa, kapena aphunzira kudziyimira pawokha. Ndipo akhoza kutitangwanitsa tikakhala pakhomo osachokapo.
**Nthawi yokumana pamaso mpamaso, kutamandira chifukwa chochita bwino, komanso kusinthasintha zochitika kumachepetsa khalidwe loipa.
Nenani chikhalidwe chomwe mukufuna kuwona Gwiritsani ntchito mawu abwino mukamamuuza mwana wanu zochita; monga 'Chonde chotsa zovala zako' (m'malo mwa 'Osawononga apa')
Zonse zili mukaperekedwe ndi kalandilidwe Kukalipira mwana wanu kumangokupangitsani inu ndi iye kupwetedwa mtima komanso kukwiya kwambiri. Mpangeni mwana wanu kukumvetserani pogwiritsa ntchito dzina lake. Lankhulani ndi mawu odekha.
Tamandani mwana wanu akakhala kuti akuchita bwino pakhalidwe lake Yesani kutamanda mwana kapena wachinyamata wanu chifukwa cha zomwe wachita bwino. Mwina sangawonetse, koma mudzaona akuchitanso zinthu zabwinozo. Zidzawatsimikizanso kuti mumatsatira zochita zawo ndikutinso mumawakonda.
Khalani zenizeni Kodi mwana wanu angachitedi zomwe mukumufunsa kuti achite? Ndi kovuta kwambiri kuti mwana akhale chete mkati mwake kwa tsiku lathunthu koma mwina atha kungokhala chete kwa mphindi 15 mukuchita chinthu china.
Thandizani mwana wanu wachinyamata kukhala wolumikizidwa Achinyamata makamaka ayenera kumalumizikizana ndi anzawo. Thandizani mwana wanu wachinyamata kulumikizidwa ku masamba a mchezo ndinjira zina zokhala motalikirana zimene zili zotetezedwa. Izi ndizomwe mungachitire limodzi!
Kupanga zothana ndi mchitidwe woyipa Yesani njira zitatu izi kuti muthane ndi zoyipa m'nyumba mwanu:
- Kupeza njira ina Letsani zisanayambe! Akayamba kusakhanzikika, mutha kuwasokoneza ndi chinthu chosangalatsa kapena choseketsa: "Bwerani, tiyeni tipite panja tikayende!"
- Gwiritsani ntchito zotsatira zake Kugwiritsa ntchito Zotsatira kumathandizira kuphunzitsa ana athu kutenga udindo pa zotsatira za zomwe amachita. Amaloleranso kulangidwa kowongoledwa. Izi ndizothandiza kwambiri kuposa kumenya kapena kukalipa. Mpatseni mwana wanu chisankho chotsatira malangizo anu musanamupatse zotsatira. Yesetsani kukhala odekha mukamapereka zotsatira, onetsetsani kuti ndi zomwe mungatsatire, ndipo zikatha, pezani njira yoyamikirira mwana wanu pazabwino zomwe wachita.
- Pumirani Mukumva ngati mukufuna kukuwa? Dzipatseni masekondi khumi (10) opumira. Pumirani mkati ndi kunja pang'onopang'ono kasanu. Kenako yesani kuyankha modekha.