Mmene Tingapewere Kusalana komanso Kufalitsa Mauthenga Abodza
Mmene tingachitirepo kanthu ngati wina akufalitsa mauthenga abodza
Pakali pano anthu ambiri ndi amantha komanso ankhawa - ndipo mu nthawi yovuta ngati imeneyi, anthu ena amafalitsa mauthenga abodza. Nthawi zambiri, anthu oterewa samachita izi mwakufuna koma kumakhala kufuna kuthandiza - kungoti samadziwa komwe angakapeze mauthenga olondola.
Zomwe tingachite ngati m'bale wathu kapena mnzathu akufalitsa mauthenga osalondola:
- Mutha kuyamba ndi kuwayankhulira pambali - kapena kuwatumizira uthenga wa pa lamya. M'baleyu atha kukumvetsetsani mukatere kusiyana ndikuwayankhula moyalutsa manyazi pagulu.
- Musawadzudzule kuti akufalitsa mauthenga abodza. Auzeni kuti komwe kukuchokera zomwe anafalitsa kukhala ngati sikodalilika kwenikweni kapena kuti uthenga womwe anafalitsa ukuoneka ngati siwolondola kwenikweni.
- Auzeni kuti adzitha kupeza mauthenga kuchokera ku mabungwe odalirika monga UNICEF kapena bungwe loona za umoyo padziko lonse lapansi la WHO, ndipo muwalimbikitse kuti adzitsatira mabungwe amenewa akafuna kupeza mauthenga atsopano komanso otsimikizika.
Mnene tingachitirepo kanthu ngati wina akulimbikitsa zosalana
Palibe chifukwa chogwira mtima chosalirana kapena kusankhana potengera dziko lomwe munthu akuchokera munyengo ya milili kapena nthawi ina iliyonse. COVID-19 amatha kukhudza munthu wina aliyense posatengera komwe akuchokera, momwe akuonekera, kapena zaka zakubadwa. Anthu othawa kwawo chifukwa cha mavuto osiyanasiyana ndi amodzi mwa anthu omwe amakhala pachiwopsezo chachikulu. Matenda a COVID-19 sasankha, ndipo nafenso tikamapereka chithandizo sitikuyenera kusankha.
Zomwe tingachite ngati wachibale kapena mnzathu akulimbikitsa zosalana:
- Tikubwerezanso kuti yambani ndi kuwayankhulira pambali- kapena kuwatumizira uthenga wa pafoni. M'baleyu atha kukumvetsetsani mukatere kusiyana ndi kumuyankhula momuyalutsa pagulu.
- Aunikireni kuti munthu wina aliyense atha kutenga tizilombo ta mavayilasi osati anthu amtundu umodzi basi.
- Aunikireninso potsindika kuti kuganiza kuti anthu a mtundu umodzi ndi amene akufalitsa kachilomboka kutha kubweretsa mavuto aakulu - kutha kulimbikitsa m'chitidwe wa nkhaza komanso kuletsa anthu kuti asamapite kuchipatala pamene akufunikira kutero, ndipo izi zingalimbikitse kufala kwa matendawa.
- Auzeni kuti munthawi ngati iyi, ndipofunika kuthandizana komanso kulimbikitsa mtima wa chikondi - ngakhale tikukhala mwamantha.