Spread Awareness

Falitsani Mauthenga a COVID-19 ndipo Chitanipo Kanthu

Mnene INU mungathandizirepo

2 minutes

1. Pezani mauthenga atsopano pa masamba a pa intaneti a UNICEF komanso a bungwe loona za umoyo dziko lonse la WHO

DZIWANI IZI: Mudzadulidwa mayunitsi mukalowa pa masambawa, mogwirizana ndi mitengo ya intaneti yomwe mumagwiritsa ntchito.

2. Tumizirani Anzanu Mauthengawa

Tumizani mauthenga komanso zithunzi zomwe mukupeza pa masamba a UNICEF ndi WHO pa tsamba lanu la Facebook, pa WhatsApp, pa Tiktok, pa Snapchat, pa Instagram, pa Twitter (ndi masamba onse amchezo a pa intaneti amene mumagwiritsa ntchito) poonetsetsa kuti anzanu akupeza mauthenga olondola.

Tsamba la intaneti lili mmusili likuthandizani kupeza mauthenga olondola, koma osaiwala kutumizira anzanu!

Tumizirani ena masamba a intaneti amenewa pa masamba omwe mumakumanirana ndi anzanu kapena kudzera mu ndemanga zomwe mumalemba pa masamba omwe mumalowalowa.

3. Lembetsani kuti mukhale membala wa tsamba la U-Report kuti mupeze mauthenga atsopano m'dziko lanu komanso kuti mudziwe njira zabwino zodzitetezera

Tsamba la U-Report COVID-19 Information Chatbot limakhala ndi mauthenga ofunikira okhudza COVID-19

five minutes

1. Kudziyesa pa zomwe mukudziwa

Kodi mukudziwa zokhudza COVID-19? Yeserani kuyankha mafunso otsatirawa ofunsidwa ndi a UNICEF. Mukamaliza, mutha kuwafunsa anzanu kuti nawo ayesere kuyankha. .

2. Tsekulani tsamba la intaneti la VOICES OF YOUTH kuti mupeze nkhani, ndakatulo, zojambulajambula, komanso makatuni zolembedwa ndi kujambulidwa ndi achinyamata kufotokoza zomwe aziona mnyengo ya mliri wa COVID-19. Lowani pa tsambali ndipo nanunso mutha kuikapo nkhani, zolembalemba kapena zojambula zanu, kapena mutha kuona zinthu zosiyanasiyana pa Twitter potsekula tsamba la Voices of Youth on Twitter.

3. Ikani ma vidiyo oonetsa zomwe mukuchita pa nthawi imeneyo

Ikani ma vidiyo oonetsa momwe munthu angasambire m'manja kapena kupereka mauthenga a ubwino wokhala motalikirana ndi anzanu. Onetsetsani kuti muli ndi mauthenga olondola musanafalitse kwa anzanu - mutha kupeza mauthenga ambiri pa tsamba la pa intaneti la UNICEF UNICEF's website. Muthanso kutenga nawo gawo pa zambiri zomwe zikuchitika m'masamba a intaneti amchezo pofuna kulimbikitsa umoyo wabwino komanso kudziteteza ku COVID-19, kapenanso kulimbikitsa anthu.

4. Phunzitsani anzanu

Ngati muli ndi luso loti mutha kulipanga kunyumba kwanu popanda kudziika pachiopsezo (monga kuphika, kuvina, kulakatula ndakatulo, masewera olimbitsa thupi, zojambulajambula) mutha kujambula ndikutumizira anzanu ngati njira imodzi yowasangalatsira komanso kudzisangalatsa nokha m'nyengo imeneyi.

5. Lowereranipo

Yankhulanipo ngati mwaona kapena kumva kuti m'bale wanu akufalitsa mauthenga osatsimikizika kapena abodza.

15+ minutes

1. Yankhulani ndi abale anu

Onetsetsani kuti aliyense m'banja mwanu akudziwa ubwino wosamba m'manja komanso kukhala munthu waukhondo, kukhala motalikirana wina ndi mnzake, komanso komwe angapeze mauthenga olondola komanso otsimikizika. Itanitsani mkumano wa pabanja pomwe ungakambirane izi. Ngati muli ndi achibale omwe sakukhala ndi inu komanso alibe komwe atha kupeza mauthenga odalirika, mudziwayimbira foni. Izi zimafunika makamaka kwa achibale omwe ndi achikulire (oposa zaka 70) komanso ena omwe ali pa chiopsezo chachikulu.

2. Thandizirani ku mbali ya sukulu komanso masewera

Funsani ngati mungathandize pophunzitsa ana anu kapena kuchita masewera osiyanasiyana ngati anawa anatsekera sukulu.

3. Kuwerenga ndi anzanu

Ngati sukulu yanu ya sekondale kapena yaukachenjede munatsekera, lumikizanani ndi anzanu kudzera pa foni kapena pa intaneti kuti mudzitha kuchitira limodzi ntchito zosiyanasiyana za ku sukulu aliyense ali kwawo. Kuphunizira kotere kumakhala kovuto kwa anthu ena omwe anazolowela kuthandizana maso ndi maso ndipo samakhala omasuka kufunsa pomwe sakumvetsa.

4. Kuchitira zinthu pamodzi

Konzani zochitika ndi anzanu, achibale kapena anthu oyandikana nawo polumikizana pa foni kapena pa intaneti poonetsa umodzi komanso kugwirana manja munthawi ya mliriwu. M'mayiko ena, anthu amatha kuyimbira nyimbo limodzi kapena kuliza zida zoyimbira nyimbo limodzi ndi oyandikana nawo nyumba - koma aliyense ali m'nyumba mwake.

5. Mavuto am'dera mwanu

N'kutheka kuti ndinu kale membala wa limodzi mwa magulu opezeka m'dera lanu - ngati zili choncho, mutha kumachitira zinthu limodzi ndi anzanu kuti mudziwe momwe anthu am'dera lanu akumvera munyengo imeneyi, zosowa zawo, komanso nkhawa zawo. Mutha kugwiritsa ntchito magulu a pa WhatsApp a anthu am'dera lanu, masamba a pa Facebook, listserv, ngakhalenso kuimbirana mafoni kuti mukambirane ndi anthu ena komanso kuti mukhale ndi mndandanda wa zosowa komanso nkhawa zomwe anthu am'deramo ali nazo. Izi zikhoza kutumizidwa kwa atsogoleri am'madera kuti mwina athe kulowererapo. Ngati simuli m'gulu lililonse m'dera lanu, fufuzani kuti ndi magulu ati amene alipo, omwe inuyo mutha kulowa nawo.

Kupita patsogolo