Kukhala ndi HIV munyengo ya Covid-19.
Kodi anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV ali ndi chiopsezo chochulukirapo chodwala COVID-19?
Pakali pano, tilibe umboni wokwanira wokhudza chiopsezo cha COVID-19 pakati pa anthu omwe ali ndi kachilombo ka HIV. Anthu omwe ali pachiopsezo chochulukirapo chodwalika kwambiri akatenga matenda a COVID-19 ndi omwe ali achikulire, munthu aliyense yemwe ali ndi vuto la matenda ena, komanso anthu omwe chitetezo chawo cha m'thupi chili chotsika. N'chifukwa chake kuli koyenera kutsata malangizo a momwe tingadzitetezere ku COVID-19 komanso kulandira chithandizo mwamsanga tikawonetsa zizindikiro za COVID-19.
Ndingatani kuti ndikhale wokonzeka?
- Onetsetsani kuti mukumakhala ndi mankhwala oti atha kukwanira kumwa kwa masiku 30 nthawi zonse.
- Sungani ma ARV okwanira miyezi itatu kufikira isanu ndi umodzi nthawi yomwe m'dziko mwakhazikitsidwa malamulo oletsa kuyendayenda kufikira pomwe malamulowa adzasiye kugwira ntchito. Ngati mankhwala anu akupita kokutha ndipo mukulephera kupeza ena, yankhulani ndi azachipatala kuti akuthandizeni kuti mudzipeza mankhwala mofulumira kuopetsa kusokoneza ndondomeko yanu ya kamwedwe ka mankhwala..
- Musamamwe mankhwala anu modukizadukiza ndi cholinga choti akhale nthawi yaitali.
- Ma ARV amasiyana, choncho musamwe ma ARV anzanu.
- Onetsetsani kuti mwalandira akatemera onse oyenera panthawi yoyenera.
- Khalani ndi dongosolo loti achibale kapena anzanu adzakuthandizeni ngati mwadwala ndipo simungakwanitse kuchoka panyumba panokha.
- Onetsetsani kuti mukutha kuyankhulana ndi azachipatala powayimbira foni kapena kudzera pa mauthenga a pafoni.
- Khalani osamala nthawi zonse ndipo mudzitha kulumikizana ndi achibale, anzanu komanso anthu ena omwe angakuthandizeni zitakuvutani
Kodi ndikatenga COVID-19 ndipo ndili ndi HIV, ndili pachiopsezo chokulirapo chodwalika kwambiri ndi kumwalira?
Pali zambiri zomwe akatswiri asayansi ndi madotolo sakudziwa pakali pano, kuphatikizapo yankho la funso lafunsidwa apali. Komabe, chomwe tikudziwa ndi chakuti anthu omwe ali ndi chitetezo cha mthupi chotsika amavutika kuti athane ndi tizolombo toyambitsa matenda osiyanasiyana kuphatikizapo COVID-19. Popanda ma ARV, kachilombo ka HIV kamachepetsa chitetezo cha m'thupi. Ndi chifukwa chake mukuyenera kupitiriza kumwa ma ARV kuti chitetezo chanu cham'thupi chikhale champhamvu.
Kodi n'kotheka kupita ku chipatala kapena kukakumana ndi azachipatala?
Yankho la funsoli litha kutengera mmene zinthu zilili m'dziko mwanu. Choyamba kuchita ndi kufunsa ku chipatala kwanu kuti mudziwe mmene anthu omwe ali ndi vuto ngati lanu akumathandizidwira. Ngati kuli kotheka, njira yabwino kwambiri yopeza chithandizo cha ku chipatala ndi kudzera pa foni. Ngati chipatala chomwe mumakalandilako chithandizo chili kutali kwambiri, panyengo imeneyi mukhoza kuyamba kulandira chithandizo pa chipatala chomwe chakuyandikirani. M'maiko ena, ngati munthu uli ndi chitetezo chokwanira cham'thupi sumayenera kupita kuchipala pafupipafupi ndipo kumakhala kotheka kukupatsa ma ARV okwanira kumwa kwa nthawi yaitali. Imbani foni ku chipatala kwanu chifukwa ndikotheka mutha kulandira chithandizo chanu pa foni pompo. Onetsetsani kuti mwapereka keyala yanu komanso nambala ya foni yanu ku chipatala kuti adzitha kukupezani mosavuta. Onetsetsaninso kuti muli ndi nambala ya foni ya kuchipatala kuti mudzitha kuyimba mukafuna chithandizo. Ngati pakufunikira kuti mupite kuchipatala ndipo muyenda pa galimoto za matola, tsatirani ndondomeko zonse zopewera COVID-19 kuti mukhale otetezeka. Nthawi zina pakhoza kufunika kuti mukhale ndi kalata kapena umboni osonyeza kuti mukuyenera kukakumana ndi dotolo - funsani achipatala ngati izi zingafunikire.
Kodi ndingatani pamene ma ARV anga akupita kokutha?
Ngati ma ARV akupita kukutha, chonde imbani foni ku chipatala kuti akulangizeni njira yomwe mungathandizikire. Imodzi mwa njirayi ndi kudzakupatsirani ma ARV kunyumba kwanu kapena kudzasiya ma ARV m'dera lanu. Ngati kuli kotheka, pemphani kuti akupatseni ma ARV oti atha kukwanira kumwa nthawi kwa yaitali, yosachepera miyezi itatu - makamaka ngati m'dziko mwanu akukhazikitsa malamulo oletsa anthu kuyendayenda. Ngati abale anu ena akupita kuchipatalako ndipo akudziwa za m'mene mulili m'thupi mwanu, mutha kuwatuma kuti akakutengereni ma ARV. Ngati mupite nokha kukatenga ma ARV kuchiptala, tsatirani njira zonse zodzitetezera ku COVID-19.
Kodi ma ARV atha kuchiza COVID-19?
Pakali pano kulibe mankhawala kapena katemera yemwe atha kuchiza kapena kuteteza munthu ku COVID-19. Nthawi zambiri, zizindikiro za COVID-19 sizimakhala zowopsa ndipo anthu ambiri amachira. Kafukufuku akadali mkati wofuna kupeza katemera ndi mankhwala a COVID-19.
Kodi ndikotheka kukumbatirana, kupsopsonana kapena kugonana?
Kukhudza malovu a munthu wina - monga popsopsonana, kapena kukhudzana matupi - monga pogonana - zitha kufalitsa COVID-19. COVID-19 amafala mukakhudza timadzimadzi tomwe timatuluka munthu akamalavula, kutsokomola, kupuma kapenanso kumina. Pakadali pano, palibe umboni woti COVID-19 imafalanso kudzera m'kugonana. Ngati inu ndi okondedwa anu mukukhala nyumba imodzi ndipo simukusonyeza zizindikiro za COVID-19 komanso mumatsata ndondomeko zodzitetezera ku matendawa, mutha kugonana potsata njira zodzitetezera monga kugwiritsa ntchito kondomu. Ngati makondomu kapena njira zina zolerera zikupita kokutha, imbani foni kwa a chipatala kuti akulangizeni mmene mungapezera zina.
Ngati andiyeza COVID-19, ndikoyenera kuti ndiwauze kuti ndili ndi kachilombo ka HIV?
Kuulula za momwe m'thupi mwanu mulili ndi chisankho chanu, ndipo wina aliyese asakukakamizeni kuti munene. Koma kuuza azachipatala za momwe mulili m'thupi mwanu kumathandiza kuti azachipatalawo akupatseni chithandizo choyenera. Dziwani kuti malamulo amakupatsani ufulu wosungiridwa chinsinsi, ndipo azachipatala akuyenera kuwatsatira.
Wachibale wandikwiira kwambiri - akundikalipira chifukwa choti ndili ndi HIV. Ndili ndi mantha chifukwa ndikuona ngati andivulaza, komano sitingachoke panyumba. Ndingatani pamenepa?
COVID-19 akumachitisa anthu kuti akhale a mantha, opsinjika mumtima komanso ankhawa, koma sizikuyenereza anthu kuchitirana nkhaza. Ngati mukuwona kuti muli pachiopsezo, kapena mukuchitiridwa nkhaza, muli ndi ufulu okapeza chithandizo ndikuchoka pakhomopo. Kumbukirani kuti si vuto lanu. Patha kukhala povuta kuti mudziwe komwe mungapeze chithandizo. Pezani munthu yemwe ndiwodalirika, yemwe angakuthandizeni mukamutulira nkhawa zanu zonse. Imbirani achipatala kapena ku manambala aulele komwe munthu amapeza chithandizo chosiyanasiyana kuti mupeze chithandizo.
Mukufuna kudziwa zambiri?
"* Ngati mukufuna chithandizo pa zaumoyo wogonana, tsekulani tsamba la intaneti ili: IPPF Blog * Ngati mukufuna chithandizo chokhudza umoyo wanu wam'malingaliro m'nyengo iyi ya COVID-19, werengani zomwe a UNICEF analemba potsekula tsamba la intaneti ili: UNICEF article * Pezani chithandizo pa nkhani zokhudza pathupi kapena kuyamwitsa panyengo ya COVID-19 potsekula tsamba la intaneti la bungwe loona za umoyo padziko lonse lapansi (WHO) ili: WHO komaso tsamba la UNICEF South Africa * Ngati mukufuna kuchitapo kanthu, tsekulani tsamba la intaneti la Voices of Youth"