Fun at home

Kusangalala Muli Kunyumba

Izi ndi zina zomwe mungachite kuti mudzisangalatse panthawi yomwe muli kunyumba, ndipo sizikuchita kufunikira zinthu zochuluka kuti zitheke.

book

Nkhani ya Zithunzi

  • Lingalirani za nkhani yomwe m'makonda kuimvera kapena kuifotokoza. Itha kukhala yoti inachitikadi, nthano, kapena yopeka nokha
  • Lingalirani magawo 6 ofunikira ankhaniyi, kuphatikizapo chiyambi ndi mathero ake.
  • Pindani kapepala kuti kakhala ndi magawo 6 ofanana. Jambulani magawo 6 aja m'mabokosiwo.
pencil

Pezani Ndakatulo

  • Pezani tsiku lomangomvetsera zomwe anthu omwe muli nawo pafupi amakonda kukamba. Lembani mawu kapena ziganizo zomwe mukumva iwo akunena.
  • Lembani ndakatulo polumikiza mawu kapena ziganizo zija momwe mungalumikizire..
happiness jar

Chikho cha Zabwino

  • Tolerani mauthenga achilimbikitso pamoyo wamunthu kuchokera m'mabuku omwe munawerengapo, kuchokera kwa achinyamata, kapenanso kwa akuluakulu m'dera lanu. Onjezerani nzeru zanu pa mauthenga achilimbikitsowa.
  • Lembani uthenga uliwonse pa kapepala kakang'ono ndikuponya mu chikho kapena botolo lalikulu.
  • M'mawa uliwonse, tulutsani kapepala kamodzi ndikuwerenga uthenga omwe walembedwapo, kapena awerengereni ena.
recycle

Zojambulajambula

  • Pezani nyuzipepala kapena ma magazini akale, majumbo amitundu yosiyanasiyana, kapena zigamba.
  • Ziduleni kuti zikhale tizidutsa ting'onoting'ono monga 1cm kalikonse.
  • Pangani chithunzi pomata tizidutswato pa pepala.
draw house

Lingalirani za Malo Abwino

  • Sankhani malo aliwonse m'dera lanu.
  • Lingalirani kuti mungachite chani kuti malowa akhale abwino kwa achinyamata.
  • Lambulani chithunzi chosonyeza masomphenya anuwo.
invention

Lingalirani za Chinthu Chatsopano

  • Ganizirani vuto lomwe mumakumana nalo tsiku ndi tsiku. Litha kukhala vuto lalikulu kapenanso laling'ono.
  • Lingalirani za njira yatsopano yomwe ingagwiritsidwe ntchito pochepetsa kapena kuthetsa vutolo.
  • Jambulani chithunzi cha njira yatsopano yomwe munalingalirayo. Lembani ziganizo zingapo zofotokoza zanjirayi kuti anthu ena amvetsetse mmene ingagwirire ntchito
birds eye

Kuona kwa M'mwamba ndi Kuona kwa M'munsi

  • Lingalirani mmene dera lanu lingaonekere mutakhala kuti inuyo ndinu mbalame ndipo mukuliona deralo mukuuluka m'mwamba kapena mutakhala pamwamba pamtengo.
  • Lingalirani za momwe malo omwewo angaonekere mutakhala kuti ndinu nyerere ndipo mwaima pansi. Jambulani chithunzi cha zomwe mungaone.
picture frame

Felemu ya Chithunzi

  • Pezani timiyala kapena tizidutswa ta mapepala, zomatira ndi mapepala okulirapo a nyuzipepala odulidwa mwabokosi
  • Matani timiyala kapena tizidutswa ta mapepala mozungulira malire a pepala lodulidwa mwabokosi lija. Dikirani kuti ziwume.
  • Dulani ndi kuchotsa gawo la pakati pa pepalalo ndipo gwiritsani ntchito chotsalacho ngati felemu ya chithunzi..
Kubwerera Kupita patsogolo