student

Khalani Katswiri Wophunzira COVID-19

Kodi pali kusiyana kotani pakati pa coronavirus ndi COVID-19?

Ma Coronavirus ndi banja la tizilombo tomwe tingayambitse matenda mwa anthu. COVID-19, pamodzi ndi SARS ndi MERS, ndi amodzi mwa mavayilasi ambiri m'banjali omwe angayambitse mavuto a kapumidwe.

Kodi zizindikiro za COVID-19 ndi ziti?

  • Kutentha thupi
  • Chimfine
  • Chifuwa
  • Kutopa
  • Kubanika popuma

Kodi COVID-19 imafalikira bwanji?

COVID-19 imafalikira kudzera m'zothamwika zing'onozing'ono zomwe simungazione. Wina akapuma, akakhosomola, kapena kuyetsemula, zothamwikazi zimayikidwa mumpweya ndipo munthu wina amatha kuzipumira mkati mwake. Zothamwikazi zikagwa kuchokera mumpweya muja zimakakhalaso pamalo, pomwe munthu akhoza kuzikhudza kenako ndikugwira nkhope, pakamwa, maso kapena mphuno. Ichi ndichifukwa chake kutalikirana ndi kusamba m'manja pafupipafupi ndikusamba m'manja ndi sopo ndi madzi ndikofunikira.

Kodi mliri ndi chiyani?

World Health Organisation, kapena WHO, idalengeza kuti COVID-19 ndi mliri padziko lonse lapansi pa Marichi 12, 2020. Izi zikutanthauza kuti matendawa afalikira padziko lonse lapansi kumayiko osiyanasiyana.

Kodi kukhala motalikirana ndi chiyani?

Kukhala motalikirana kumatanthauza kupewa misonkhano yayikuluyikulu ndikukhala motalikirana muyezo wosachepera mapazi atatu (3), kapena mita imodzi (1), kuchokera kwa ena kuti tiletse kufalikira kwa COVID-19. Kuphatikiza apo, popereka moni kwa wina, khalani motalikirana muja ndipo pewani kugwirana chanza, kupsompsonana, ndi kukumbatirana. Pewani kugwiritsa ntchito mayendedwe omwe aliyense amagwiritsa ngati zili zosafunikira, ngati musakumva bwino m’thupi, khalani kunyumba. Tsoka ilo, izi zikuphatikizanso achibale ndi abwenzi omwe simukukhala nawo. Lumikizanani wina ndi mzake pogwiritsa ntchito maluso amakono monga mafoni ndi masamba a mchezo.

Kodi asymptomatic amatanthauza chiyani?

Asymptomatic amatanthawuza kuti munthu akumva bwino komanso kuwoneka wathanzi koma ali ndi kachilombo ndipo akhoza kupatsira ena. Ngakhale anthu opanda zizindikilo amatha kufalitsa COVID-19, chomwe chili chifukwa chinanso chokhalira motalikirana.

Kodi nthenda ya COVID-19 imatenga nthawi yayitali bwanji ndipo ndingayambe kuyipatsira liti?

Zizindikiro nthawi zambiri zimatha masiku 5-7 koma mutha kufalitsa matendawa masiku 2 - 14 musanayambe kudwala. Komabe, anthu amatha kudwala kwa milungu iwiri kapena kupitilira apo, kutengera zaka za munthuyo ndi momwe m'thupi mwake mulili. Anthu omwe akudwala ayenera kudzipatula okha.

Kodi ndichite chiyani ndi uthengawu?

Tsopano popeza ndinu katswiri, gawani nzeru zanu zatsopano ndi abwenzi ndi abale!

Kubwerera