Dzitetezeni pa nyengo ya mvula
- Pamene mvula yochuluka ikugwa m’madera ambiri, mverani mauthenga a zanyengo kuti mudziwe nthawi yomwe mvula yamphamvu ingagwe mdera lanu ndikupewa ngozi za madzi osefukira.
- Thawirani msanga kumalo okwera pomwe mwaona zizindikiro zoti madzi atha kusefukira. Mvula ya mphamvu ndi chimodzi mwa zizindikiro za kusefukira kwa madzi.
- Makolo, phunzitsani ana anu za kuopsa kosewera kapena kuoloka m’malo omwe madzi asefukira.
- Khalani atcheru ndi madzi osefukira mu nyengo ya mvula. Madzi atha kusefukira nthawi yomwe sitikuyembekezera.
- Musayandikire mawaya a magetsi omwe agwa. Kaneneni ku Escom, ku polisi kapena kwa amfumu za mawaya a magetsi omwe agwa.
- Ngakhale angawoneke kuti ndi oyera, madzi akhoza kukhala ndi tizilombo toyambitsa matenda a cholera. Imwani madzi owilitsa kapena kuthila mankhwala a chlorine.
- Sungani makalata onse ofunikila monga chiphaso chakubadwa mupepala la plastic momwe simungalowe madzi. Phunzilani zambiri zokhudza cholera.
- Chonde uzani anzanu zauthengawu kuti muthandize kupulumutsa moyo wawo. Nawonso angakhale U-Reporter potumiza JOIN ku 1177. Zonsezi mzaulere pa TNM ndi Airtel!