2 climate

Dzitetezeni pa nyengo ya mvula

  1. Pamene mvula yochuluka ikugwa m’madera ambiri, mverani mauthenga a zanyengo kuti mudziwe nthawi yomwe mvula yamphamvu ingagwe mdera lanu ndikupewa ngozi za madzi osefukira.
  2. Thawirani msanga kumalo okwera pomwe mwaona zizindikiro zoti madzi atha kusefukira. Mvula ya mphamvu ndi chimodzi mwa zizindikiro za kusefukira kwa madzi.
  3. Makolo, phunzitsani ana anu za kuopsa kosewera kapena kuoloka m’malo omwe madzi asefukira.
  4. Khalani atcheru ndi madzi osefukira mu nyengo ya mvula. Madzi atha kusefukira nthawi yomwe sitikuyembekezera.
  5. Musayandikire mawaya a magetsi omwe agwa. Kaneneni ku Escom, ku polisi kapena kwa amfumu za mawaya a magetsi omwe agwa.
  6. Ngakhale angawoneke kuti ndi oyera, madzi akhoza kukhala ndi tizilombo toyambitsa matenda a cholera. Imwani madzi owilitsa kapena kuthila mankhwala a chlorine.
  7. Sungani makalata onse ofunikila monga chiphaso chakubadwa mupepala la plastic momwe simungalowe madzi. Phunzilani zambiri zokhudza cholera.
  8. Chonde uzani anzanu zauthengawu kuti muthandize kupulumutsa moyo wawo. Nawonso angakhale U-Reporter potumiza JOIN ku 1177. Zonsezi mzaulere pa TNM ndi Airtel!