Kumva Kusungulumwa

Kulimbana ndi COVID-19

Kusungulumwa komanso kuchita mantha pakadali pano ndizabwinonwino. Izi ndi zomwe munthu umayembekezera kuchitika munyengo yomwe mwapezeka muli inuyi. Dziwani kuti pamene mukuda nkhawa komanso kusungulumwa, simuli nokha.

Chitani zodzisamalira nokha pakuchita izi:

  • Kudzuka msanga ndikudya chakudya cham'mawa chopatsa thanzi
  • Kuchita masewera olimbitsa thupi
  • Kuwerenga
  • Kulumikizana ndi abwenzi anu kudzera pa masamba a mchezo
  • Kuthandiza anzanu omwenso amasungulumwa
  • Ngati alipo, kuchita makalasi anu apa intaneti ndikumaliza ntchito zomwe akupatsani ku sukulu yanu nthawi yoyenelera
  • Kupeza njira yofotokozera malingaliro anu kudzera mu ndakatulo kapena kulemba mu dayale
  • Kupanga zaluso
  • Kuyesa kuchita masewera olimbitsa thupi musanakagone
  • Kupita kukagona mwansanga

Musaiwale kufikira munthu amene mumamukhulupirira ndikumudziwitsa za momwe mukumvera. Munthu wake akhoza kukhala kholo, gogo, bwenzi kapena mphunzitsi.

Kubwerera Kupita patsogolo