Kusangalala Muli Kunyumba
Izi ndi zina zomwe mungachite kuti mudzisangalatse panthawi yomwe muli kunyumba, ndipo sizikuchita kufunikira zinthu zochuluka kuti zitheke.
Nkhani ya Zithunzi
- Lingalirani za nkhani yomwe m'makonda kuimvera kapena kuifotokoza. Itha kukhala yoti inachitikadi, nthano, kapena yopeka nokha
- Lingalirani magawo 6 ofunikira ankhaniyi, kuphatikizapo chiyambi ndi mathero ake.
- Pindani kapepala kuti kakhala ndi magawo 6 ofanana. Jambulani magawo 6 aja m'mabokosiwo.
Pezani Ndakatulo
- Pezani tsiku lomangomvetsera zomwe anthu omwe muli nawo pafupi amakonda kukamba. Lembani mawu kapena ziganizo zomwe mukumva iwo akunena.
- Lembani ndakatulo polumikiza mawu kapena ziganizo zija momwe mungalumikizire..
Chikho cha Zabwino
- Tolerani mauthenga achilimbikitso pamoyo wamunthu kuchokera m'mabuku omwe munawerengapo, kuchokera kwa achinyamata, kapenanso kwa akuluakulu m'dera lanu. Onjezerani nzeru zanu pa mauthenga achilimbikitsowa.
- Lembani uthenga uliwonse pa kapepala kakang'ono ndikuponya mu chikho kapena botolo lalikulu.
- M'mawa uliwonse, tulutsani kapepala kamodzi ndikuwerenga uthenga omwe walembedwapo, kapena awerengereni ena.
Zojambulajambula
- Pezani nyuzipepala kapena ma magazini akale, majumbo amitundu yosiyanasiyana, kapena zigamba.
- Ziduleni kuti zikhale tizidutsa ting'onoting'ono monga 1cm kalikonse.
- Pangani chithunzi pomata tizidutswato pa pepala.
Lingalirani za Malo Abwino
- Sankhani malo aliwonse m'dera lanu.
- Lingalirani kuti mungachite chani kuti malowa akhale abwino kwa achinyamata.
- Lambulani chithunzi chosonyeza masomphenya anuwo.
Lingalirani za Chinthu Chatsopano
- Ganizirani vuto lomwe mumakumana nalo tsiku ndi tsiku. Litha kukhala vuto lalikulu kapenanso laling'ono.
- Lingalirani za njira yatsopano yomwe ingagwiritsidwe ntchito pochepetsa kapena kuthetsa vutolo.
- Jambulani chithunzi cha njira yatsopano yomwe munalingalirayo. Lembani ziganizo zingapo zofotokoza zanjirayi kuti anthu ena amvetsetse mmene ingagwirire ntchito
Kuona kwa M'mwamba ndi Kuona kwa M'munsi
- Lingalirani mmene dera lanu lingaonekere mutakhala kuti inuyo ndinu mbalame ndipo mukuliona deralo mukuuluka m'mwamba kapena mutakhala pamwamba pamtengo.
- Lingalirani za momwe malo omwewo angaonekere mutakhala kuti ndinu nyerere ndipo mwaima pansi. Jambulani chithunzi cha zomwe mungaone.
Felemu ya Chithunzi
- Pezani timiyala kapena tizidutswa ta mapepala, zomatira ndi mapepala okulirapo a nyuzipepala odulidwa mwabokosi
- Matani timiyala kapena tizidutswa ta mapepala mozungulira malire a pepala lodulidwa mwabokosi lija. Dikirani kuti ziwume.
- Dulani ndi kuchotsa gawo la pakati pa pepalalo ndipo gwiritsani ntchito chotsalacho ngati felemu ya chithunzi..